Nikwera mfumu kunka kunyumba ya Yehova, ndi amuna onse a Yuda, ndi onse okhala mu Yerusalemu pamodzi naye, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi anthu onse aang'ono ndi aakulu; nawerenga iye m'makutu mwao mau onse a m'buku la chipangano adalipeza m'nyumba ya Yehova.