Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 24:32 - Buku Lopatulika

32 Ndipo anati wina kwa mnzake, Mtima wathu sunali wotentha m'kati mwathu nanga m'mene analankhula nafe m'njira, m'mene anatitsegulira malembo?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Ndipo anati wina kwa mnzake, Mtima wathu sunali wotentha m'kati mwathu nanga m'mene analankhula nafe m'njira, m'mene anatitsegulira malembo?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Tsono iwo adayamba kukambirana kuti, “Zoonadi ndithu, mitima yathu inachita kuti phwii, muja amalankhula nafe panjira paja, nkumatitanthauzira Malembo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Iwo anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi mitima yathu sinali kutentha mʼkati mwathu pamene Iye ankayankhulana nafe pa njira ndi mmene anatitsekulira malemba?”

Onani mutuwo Koperani




Luka 24:32
14 Mawu Ofanana  

Pomlingirira Iye pandikonde; ndidzakondwera mwa Yehova.


Mtima wanga unatentha m'kati mwa ine; unayaka moto pakulingirira ine. Pamenepo ndinalankhula ndi lilime langa,


Chitsulo chinola chitsulo; chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake.


Mafuta ndi zonunkhira zikondweretsa mtima, ndi ubwino wa bwenzi uteronso pakupangira uphungu.


Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akuchirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m'mawa ndi m'mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.


Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine chikondwero ndi chisangalalo cha mtima wanga; pakuti ndatchedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu.


Ndipo ngati nditi, Sindidzamtchula Iye, sindidzanenanso m'dzina lake, pamenepo m'mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m'mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.


Kodi mau anga safanafana ndi moto? Ati Yehova, ndi kufanafana ndi nyundo imene iphwanya mwala?


ndipo sanalankhule nao wopanda fanizo: koma m'tseri anatanthauzira zonse kwa ophunzira ake.


Ndipo anawatsegulira mitima yao, kuti adziwitse malembo;


Wopatsa moyo ndi mzimu; thupi silithandiza konse. Mau amene ndalankhula ndi inu ndiwo mzimu, ndi moyo.


Ndipo pamene adampangira tsiku, anadza kunyumba yake anthu ambiri; amenewo anawafotokozera, ndi kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zochokera m'chilamulo cha Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo.


Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa