Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 23:2 - Buku Lopatulika

2 Nikwera mfumu kunka kunyumba ya Yehova, ndi amuna onse a Yuda, ndi onse okhala mu Yerusalemu pamodzi naye, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi anthu onse aang'ono ndi aakulu; nawerenga iye m'makutu mwao mau onse a m'buku la chipangano adalipeza m'nyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Nikwera mfumu kunka kunyumba ya Yehova, ndi amuna onse a Yuda, ndi onse okhala m'Yerusalemu pamodzi naye, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi anthu onse ang'ono ndi akulu; nawerenga iye m'makutu mwao mau onse a m'buku la chipangano adalipeza m'nyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ndipo mfumuyo idapita ku Nyumba ya Chauta pamodzi ndi anthu onse a ku Yuda, nzika zonse za mu Yerusalemu, ansembe ndi aneneri, ndiponso anthu onse aakulu ndi aang'ono omwe. Tsono iye adaŵerenga pamaso pao mau onse a m'buku lija la chipangano limene lidaapezeka m'Nyumba ya Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mfumuyo inapita ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi anthu onse a ku Yuda, ndi onse okhala mu Yerusalemu, ansembe ndi aneneri, ndiponso anthu ena onse kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu. Mfumuyo inawerenga mawu onse a mʼBuku la Chipangano limene linapezeka mʼNyumba ya Yehova, anthu onse akumva.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 23:2
18 Mawu Ofanana  

Ndipo anachititsa khungu m'maso mwa anthu amene anali pakhomo pa nyumba, aang'ono ndi aakulu, ndipo anavutika kufufuza pakhomo.


Munalibe kanthu m'likasamo koma magome awiri aja a mwala Mose anawalongamo pa Horebu, pamene Yehova anapangana ndi ana a Israele, potuluka iwo m'dziko la Ejipito.


Ndipo Hilikiya mkulu wa ansembe anati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la chilamulo m'nyumba ya Yehova. Napereka Hilikiya bukulo kwa Safani, iye naliwerenga.


ndi kuti yense wosafuna Yehova Mulungu wa Israele aphedwe, ngakhale wamng'ono kapena wamkulu, wamwamuna kapena wamkazi.


Ndipo anaphunzitsa mu Yuda ali nalo buku la chilamulo la Yehova, nayendayenda m'mizinda yonse ya Yuda, naphunzitsa mwa anthu.


Tsiku lomwelo anawerenga m'buku la Mose m'makutu a anthu, napeza m'menemo kuti Aamoni ndi Amowabu asalowe mu msonkhano wa Mulungu kunthawi yonse;


Naimirira poima pao, nawerenga m'buku la chilamulo cha Yehova Mulungu wao limodzi la magawo anai a tsiku; ndi limodzi la magawo anai anawulula, napembedza Yehova Mulungu wao.


Atatha masikuwa, mfumu inakonzera madyerero anthu onse okhala m'chinyumba cha ku Susa, aakulu ndi aang'ono, masiku asanu ndi awiri, ku bwalo la munda wa maluwa wa ku chinyumba cha mfumu;


Ang'ono ndi akulu ali komwe; ndi kapolo amasuka kwa mbuyake.


Adzadalitsa iwo akuopa Yehova, aang'ono ndi aakulu.


Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, mfumu Zedekiya atapangana pangano ndi anthu onse amene anali pa Yerusalemu, kuti awalalikire iwo ufulu;


Pamenepo pothandizidwa ndi Mulungu, ndiimirira kufikira lero lino, ndi kuwachitira umboni ang'ono ndi akulu, osanena kanthu kena koma zimene aneneri ndi Mose ananena zidzafika;


Landirani buku ili la chilamulo, nimuliike pambali pa likasa la chipangano la Yehova Mulungu wanu, likhale komweko mboni yakutsutsa inu.


Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aang'ono alinkuima kumpando wachifumu; ndipo mabuku anatsegulidwa; ndipo buku lina linatsegulidwa, ndilo la moyo; ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m'mabuku, monga mwa ntchito zao.


nagwira akazi ndi onse anali m'mwemo, aakulu ndi aang'ono; sanaphe mmodzi, koma anawatenga, namuka.


Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mzindawo ndi kusautsa kwakukulu; ndipo anazunza anthu a mzindawo, aakulu ndi aang'ono; ndi mafundo anawabuka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa