Ndi pambali pao anakonza Refaya mwana wa Huri, ndiye mkulu wa dera lina la dziko la Yerusalemu.
Nehemiya 3:12 - Buku Lopatulika Ndi pambali pake anakonza Salumu mwana wa Halohesi, mkulu wa dera lina la dziko la Yerusalemu, iye ndi ana ake akazi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi pambali pake anakonza Salumu mwana wa Halohesi, mkulu wa dera lina la dziko la Yerusalemu, iye ndi ana ake akazi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambali pa iyeyo Salumu, mwana wa Halohesi, wolamulira theka lina la dera la mzinda wa Yerusalemu, adakonza chigawo china, iyeyo pamodzi ndi ana ake aakazi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Salumu mwana wa Halohesi wolamulira theka la chigawo cha Yerusalemu, anakonzanso chigawo chotsatana nawo mothandizidwa ndi ana ake akazi. |
Ndi pambali pao anakonza Refaya mwana wa Huri, ndiye mkulu wa dera lina la dziko la Yerusalemu.
Odikira: ana a Salumu, ana a Atere, ana a Talimoni, ana a Akubu, ana a Hatita, ana a Sobai, zana limodzi mphambu makumi atatu kudza asanu ndi atatu.
Ndi akazi onse a mtima waluso anapota ndi manja ao, nabwera nalo thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
Inde, ndikupemphaninso, mnzanga wa m'goli woona, muthandize akazi awa amene anakangalika nane pamodzi mu Uthenga Wabwino, pamodzi ndi Klemensinso, ndi otsala aja antchito anzanga, amene maina ao ali m'buku la Moyo.