Mlaliki 7:3 - Buku Lopatulika Chisoni chiposa kuseka; pakuti nkhope yakugwa ikonza mtima. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chisoni chiposa kuseka; pakuti nkhope yakugwa ikonza mtima. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chisoni nchabwino kupambana chimwemwe, chifukwa ngakhale nkhope ikhale yakugwa, mtima umathabe kutolapo nzeru. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chisoni nʼchabwino kusiyana ndi kuseka, pakuti nkhope yakugwa ndi yabwino chifukwa imakonza mtima. |
Nati, Munthu wokondedwatu iwe, Usaope, mtendere ukhale nawe; limbika, etu limbika. Ndipo pamene ananena ndi ine ndinalimbikitsidwa, ndinati, Anene mbuye wanga; pakuti mwandilimbikitsa.
Odala inu akumva njala tsopano; chifukwa mudzakhuta. Odala inu akulira tsopano; chifukwa mudzaseka.
Tsoka inu okhuta tsopano! Chifukwa mudzamva njala. Tsoka inu, akuseka tsopano! Chifukwa mudzachita maliro ndi kulira misozi.
Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero;