Mika 7:5 - Buku Lopatulika Musakhulupirira bwenzi, musatama bwenzi loyanja; usamtsegulire pakhomo pakamwa pako, ngakhale kwa iye wogona m'fukato mwako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Musakhulupirira bwenzi, musatama bwenzi loyanja; usamtsegulire pakhomo pakamwa pako, ngakhale kwa iye wogona m'fukato mwako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Wina asakhulupirire mnansi, asadalire bwenzi lake lapamtima. Aliyense achenjere ndi pakamwa pake, ngakhale polankhula ndi mkazi wake yemwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Usadalire mnansi; usakhulupirire bwenzi. Usamale zoyankhula zako ngakhale kwa mkazi amene wamukumbatira. |
Ngakhale bwenzi langa lenileni, amene ndamkhulupirira, ndiye amene adadyako mkate wanga, anandikwezera chidendene chake.
Ndipo apinda lilime lao ngati uta wao, liname; koma akula mphamvu m'dzikomo, koma si pachoonadi; pakuti alinkunkabe nachita zoipa, ndipo sandidziwa Ine, ati Yehova.
Muchenjere naye yense mnansi wake, musakhulupirire yense mbale wake; pakuti abale onse amanyenga, ndipo anansi onse adzayenda ndi maugogodi.
Uliralira usiku; misozi yake ili pa masaya ake; mwa onse amene anaukonda mulibe mmodzi wakuutonthoza: Mabwenzi ake onse auchitira ziwembu, asanduka adani ake.
Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.
Ndipo analira pamaso pake masiku asanu ndi awiriwo pochitika madyerero ao; koma kunali kuti tsiku lachisanu ndi chiwiri anamuuza, popeza anamuumiriza; ndipo anatanthauzira anthu a mtundu wake mwambiwo.