Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mateyu 9:5 - Buku Lopatulika

Pakuti chapafupi nchiti, kunena, Machimo ako akhululukidwa; kapena kunena, Tanyamuka. Nuyende?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pakuti chapafupi nchiti, kunena, Machimo ako akhululukidwa; kapena kunena, Tanyamuka. Nuyende?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chapafupi koposa nchiti, kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Dzuka, yamba kuyenda?’

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chapafupi ndi chiti kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa’ kapena kunena kuti, ‘Imirira ndipo yenda?’

Onani mutuwo



Mateyu 9:5
15 Mawu Ofanana  

Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pamphasa: ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, machimo ako akhululukidwa.


Koma kuti mudziwe kuti ali nazo mphamvu Mwana wa Munthu pansi pano za kukhululukira machimo (pomwepo ananena kwa wodwalayo), Tanyamuka, nutenge mphasa yako, numuke kunyumba kwako.


Ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao ananena ndi wodwala manjenje, Mwana, machimo ako akhululukidwa.


Ndipo Iye, pakuona chikhulupiriro chao, anati, Munthu iwe, machimo ako akhululukidwa.


Ndipo anati kwa mkazi, Machimo ako akhululukidwa.


Ndipo pa chikhulupiriro cha m'dzina lake dzina lakelo linalimbikitsa iye amene mumuona, nimumdziwa; ndipo chikhulupiriro chili mwa Iye chinampatsa kuchira konse kumeneku pamaso pa inu nonse.


Ndipo Petro anati kwa iye, Eneya, Yesu Khristu akuchiritsa iwe; uka, yalula mphasa yako. Ndipo anauka pomwepo.