Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 3:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo pa chikhulupiriro cha m'dzina lake dzina lakelo linalimbikitsa iye amene mumuona, nimumdziwa; ndipo chikhulupiriro chili mwa Iye chinampatsa kuchira konse kumeneku pamaso pa inu nonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo pa chikhulupiriro cha m'dzina lake dzina lakelo linalimbikitsa iye amene mumuona, nimumdziwa; ndipo chikhulupiriro chili mwa Iye chinampatsa kuchira konse kumeneku pamaso pa inu nonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Munthuyu, amene mukumuwona ndipo mukumdziŵa, wakhulupirira dzina la Yesu. Chikhulupirirocho chimene ali nacho mwa Yesu, ndicho chalimbitsa miyendo yake, chamchiritsa kwenikweni, monga inu nonse mukuwoneramu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Mwachikhulupiriro mʼdzina la Yesu, munthu uyu amene mukumuona ndi kumudziwa analimbikitsidwa. Mʼdzina la Yesu ndi chikhulupiriro chimene chili mwa iye chamuchiritsa kwathunthu, monga nonse mukuona.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 3:16
21 Mawu Ofanana  

Ndipo Iye anati, Idza. Ndipo Petro anatsika m'ngalawa, nayenda pamadzi, kufika kwa Yesu.


Koma Yesu potembenuka ndi kuona iye anati, Limba mtima, mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Ndipo mkaziyo anachira kuyambira nthawi yomweyo.


Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Wokhulupirira Ine, ntchito zimene ndichita Ine adzazichitanso iyeyu; ndipo adzachita zoposa izi; chifukwa ndipita Ine kwa Atate.


Ngati munthu alandira mdulidwe tsiku la Sabata, kuti chilamulo cha Mose chingapasulidwe; kodi mundikwiyira Ine, chifukwa ndamchiritsadi munthu tsiku la Sabata?


Ameneyo anamva Paulo alinkulankhula; ndipo Paulo pomyang'anitsa, ndi kuona kuti anali ndi chikhulupiriro cholandira nacho moyo,


Ndipo anachita chotero masiku ambiri. Koma Paulo anavutika mtima ndithu, nacheuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m'dzina la Yesu Khristu, tuluka mwa iye. Ndipo unatuluka nthawi yomweyo.


Koma Petro anati, Siliva ndi golide ndilibe; koma chimene ndili nacho, ichi ndikupatsa, M'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, yenda.


Ndipo anazunzuka, naimirira, nayenda; ndipo analowa pamodzi nao mu Kachisi, nayenda, nalumpha, nayamika Mulungu.


zindikirani inu nonse, ndi anthu onse a Israele, kuti m'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, amene inu munampachika pamtanda, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, mwa Iyeyu munthuyu aimirirapo pamaso panu, wamoyo.


m'mene mutambasula dzanja lanu kukachiritsa; ndi kuti zizindikiro ndi zozizwa zichitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu.


Ndipo m'mene anawaimika pakati, anafunsa kuti, Ndi mphamvu yanji, kapena m'dzina lanji, mwachita ichi inu?


ndicho chilungamo cha Mulungu chimene chichokera mwa chikhulupiriro cha pa Yesu Khristu kwa onse amene akhulupirira; pakuti palibe kusiyana;


Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe.


Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa