ndipo kwa iwo anati, Pitani inunso kumunda, ndipo ndidzakupatsani chimene chili choyenera. Ndipo iwo anapita.
Mateyu 20:5 - Buku Lopatulika Ndiponso anatuluka usana, ndimonso popendeka dzuwa, nachita chimodzimodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndiponso anatuluka usana, ndimonso popendeka dzuwa, nachita chimodzimodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwowo adapitadi. Munthu uja adapitanso pa 12 koloko masana ndi pa 3 koloko, nakachita chimodzimodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anapita. “Anatulukanso nthawi ya 12 koloko masana, ndi nthawi ya 3 koloko masananso nachita chimodzimodzi. |
ndipo kwa iwo anati, Pitani inunso kumunda, ndipo ndidzakupatsani chimene chili choyenera. Ndipo iwo anapita.
Ndipo poyandikira madzulo anatuluka, napeza ena ataima; nanena kwa iwo, Mwaimiranji kuno dzuwa lonse chabe?
Ndipo ora lachisanu ndi chimodzi panali mdima padziko lonse, kufikira ora lachisanu ndi chinai.
Nanena nao, Tiyeni, mukaone. Pamenepo anadza naona kumene anakhala; nakhala ndi Iye tsiku lomwelo; panali monga ora lakhumi.
Yesu anayankha, Kodi sikuli maora khumi ndi awiri usana? Ngati munthu ayenda usana sakhumudwa, chifukwa apenya kuunika kwa dziko lino lapansi.
ndipo pamenepo panali chitsime cha Yakobo. Ndipo Yesu, popeza analema ndi ulendo wake, motero anakhala pachitsime.
Iye anapenya m'masomphenya poyera, mngelo wa Mulungu alinkudza kwa iye, ngati ora lachisanu ndi chinai la usana, nanena naye, Kornelio.
Koma m'mawa mwake, pokhala paulendo pao iwowa, m'mene anayandikira mzinda, Petro anakwera patsindwi kukapemphera, ngati pa ora lachisanu ndi chimodzi; ndipo anagwidwa njala, nafuna kudya;
Koma Petro ndi Yohane analikukwera kunka ku Kachisi pa ora lakupembedza, ndilo lachisanu ndi chinai.