Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 10:3 - Buku Lopatulika

3 Iye anapenya m'masomphenya poyera, mngelo wa Mulungu alinkudza kwa iye, ngati ora lachisanu ndi chinai la usana, nanena naye, Kornelio.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Iye anapenya m'masomphenya poyera, mngelo wa Mulungu alinkudza kwa iye, ngati ora lachisanu ndi chinai la usana, nanena naye, Kornelio.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsiku lina dzuŵa litapendeka, nthaŵi ili ngati 3 koloko, adaona zinthu m'masomphenya. Adaona bwino ndithu mngelo wa Mulungu akubwera kwa iye nkunena kuti, “Kornelio!”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Tsiku lina, nthawi ili ngati 3 koloko masana, anaona masomphenya. Anaona bwino ndithu mngelo wa Mulungu, amene anabwera kwa iye ndi kuti, “Korneliyo.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 10:3
23 Mawu Ofanana  

Madzulo, m'mawa, ndi msana ndidzadandaula, ndi kubuula, ndipo adzamva mau anga.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ichi chomwe wanenachi ndidzachita; pakuti wapeza ufulu pamaso panga, ndipo ndikudziwa dzina lako.


Ndakuitana iwe dzina lako, chifukwa cha Yakobo mtumiki wanga ndi Israele wosankhidwa wanga; ndakuonjezera dzina, ngakhale iwe sunandidziwe Ine.


Ndipo poyandikira ora lachisanu ndi chinai, Yesu anafuula ndi mau aakulu, kunena, Eli, Eli, lama sabakitani? ndiko kunena kuti, Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?


Ndipo anamuonekera iye mngelo wa Ambuye, naimirira kudzanja lamanja la guwa la nsembe la zonunkhira.


Ndipo dzidzidzi panali pamodzi ndi mngeloyo ambirimbiri a gulu la Kumwamba, natamanda Mulungu, nanena,


Ndipo pokayikakayika Petro mwa yekha ndi kuti masomphenya adawaona akuti chiyani, taonani, amuna aja otumidwa ndi Kornelio, atafunsira nyumba ya Simoni, anaima pachipata,


Ndipo m'mene Petro analingirira za masomphenya, Mzimu anenana naye, Taona, amuna atatu akufuna iwe.


Ndipo Kornelio anati, Atapita masiku anai, kufikira monga ora ili, ndinalikupemphera m'nyumba yanga pa ora lachisanu ndi chinai; ndipo taonani, padaimirira pamaso panga munthu wovala chovala chonyezimira,


Koma m'mawa mwake, pokhala paulendo pao iwowa, m'mene anayandikira mzinda, Petro anakwera patsindwi kukapemphera, ngati pa ora lachisanu ndi chimodzi; ndipo anagwidwa njala, nafuna kudya;


ndipo anatiuza ife kuti adaona mngelo wakuimirira m'nyumba yake, ndi kuti, Tumiza anthu ku Yopa, akaitane Simoni, wonenedwanso Petro;


Pakuti anaimirira kwa ine usiku walero mngelo wa Mulungu amene ndili wake, amenenso ndimtumikira,


Koma Petro ndi Yohane analikukwera kunka ku Kachisi pa ora lakupembedza, ndilo lachisanu ndi chinai.


Koma mngelo wa Ambuye anatsegula pakhomo pa ndende usiku, nawatulutsa, nati,


Koma ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lake Ananiya; ndipo Ambuye anati kwa iye m'masomphenya, Ananiya. Ndipo anati, Ndili pano, Ambuye,


ndipo anagwa pansi, namva mau akunena naye, Saulo, Saulo, Undilondalonderanji?


Kodi siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?


atakhala wakuposa angelo, monga momwe adalowa dzina lakuposa iwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa