Mateyu 20:3 - Buku Lopatulika Ndipo anatuluka dzuwa litakwera, naona ena ataima chabe pabwalo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anatuluka dzuwa litakwera, naona ena ataima chabe pabwalo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa nthaŵi ya 9 koloko adapitanso, nakapeza ena atangokhala khale pa msika, osagwira ntchito. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Nthawi 9 koloko mmawa, anatulukanso naona ena atayimirira pa msika akungokhala. |
Taona, mphulupulu ya mng'ono wako Sodomu ndi iye, kudzikuza, kuchuluka kwa chakudya, ndi kupumula kwa mtambasali, anali nako iye ndi ana ake; ndipo sanalimbitse dzanja la wosauka ndi wosowa.
Ndipo pamene adapangana ndi antchito, pa rupiya latheka limodzi tsiku limodzi, anawatumiza kumunda wake.
ndipo kwa iwo anati, Pitani inunso kumunda, ndipo ndidzakupatsani chimene chili choyenera. Ndipo iwo anapita.
Koma pamene ambuye ake anaona kuti kulingalira kwa kupindula kwao kwatha, anagwira Paulo ndi Silasi, nawakokera kunka nao kubwalo kwa akulu,
Ndipo aphunziraponso kuchita ulesi, aderuderu; koma osati ulesi wokha, komatunso alankhula zopanda pake, nachita mwina ndi mwina, olankhula zosayenera.
kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikulowa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima.