Ndipo Yosefe anauka tulo take, nachita monga anamuuza mngelo wa Ambuye, nadzitengera yekha mkazi wake;
Mateyu 2:14 - Buku Lopatulika Ndipo iye ananyamuka natenga kamwana ndi amake usiku, nachoka kupita ku Ejipito; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye ananyamuka natenga kamwana ndi amake usiku, nachoka kupita ku Ejipito; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Yosefe adadzuka usiku womwewo, nkutenga mwanayo ndi mai wake kupita ku Ejipito. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atadzuka, Yosefe anatenga mwanayo ndi amayi ake usiku omwewo napita ku Igupto, |
Ndipo Yosefe anauka tulo take, nachita monga anamuuza mngelo wa Ambuye, nadzitengera yekha mkazi wake;
Ndipo pamene iwo anachoka, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe m'kulota, nati, Tauka, nutenge kamwanako ndi amake, nuthawire ku Ejipito, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukaononga Iko.
nakhalabe kumeneko kufikira atamwalira Herode; kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Ambuye mwa mneneri kuti, Ndinaitana Mwana wanga atuluke mu Ejipito.
Ndipo anadza kwa Iye, namuutsa, nanena, Ambuye, Ambuye, titayika. Ndipo anauka, nadzudzula mphepo ndi mafunde ake a madzi; pomwepo zinaleka, ndipo panagwa bata.