Luka 8:24 - Buku Lopatulika24 Ndipo anadza kwa Iye, namuutsa, nanena, Ambuye, Ambuye, titayika. Ndipo anauka, nadzudzula mphepo ndi mafunde ake a madzi; pomwepo zinaleka, ndipo panagwa bata. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201424 Ndipo anadza kwa Iye, namuutsa, nanena, Ambuye, Ambuye, titayika. Ndipo anauka, nadzudzula mphepo ndi mafunde ake a madzi; pomwepo zinaleka, ndipo panagwa bata. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa24 Pamenepo ophunzira aja adadza kwa Yesu namudzutsa, adati, “Ambuye, Ambuye, tikumiratu!” Iye adadzuka, naletsa mphepoyo ndi mafunde amphamvuwo. Zidalekadi ndipo padagwa bata. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero24 Ophunzira anapita ndi kukamudzutsa Iye, nati, “Ambuye, Ambuye, ife tikumira!” Anadzuka ndipo anadzudzula mphepo ndi madzi owindukawo. Namondwe anasiya, ndipo panali bata. Onani mutuwo |
Chifukwa chanji ndinafika osapeza munthu? Ndi kuitana koma panalibe wina woyankha? Kodi dzanja langa lafupika konse, kuti silingathe kuombola? Pena Ine kodi ndilibe mphamvu zakupulumutsa? Taona pa kudzudzula kwanga ndiumitsa nyanja, ndi kusandutsa mitsinje chipululu; nsomba zake zinunkha chifukwa mulibe madzi, ndipo zifa ndi ludzu.