Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 8:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo m'mene iwo anali kupita pamadzi, Iye anagona tulo. Ndipo panyanja panatsikira namondwe wa mphepo; ndipo podzala ndi madzi, analimkuopsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo m'mene iwo anali kupita pamadzi, Iye anagona tulo. Ndipo panyanja panatsikira namondwe wa mphepo; ndipo podzala ndi madzi, analimkuopsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Pamene ankaoloka Yesu adagona tulo. Tsono padauka namondwe panyanjapo, mpaka chombo chija chidayamba kudzaza ndi madzi ndipo iwo anali pafupi kumira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Akuwoloka, Iye anagona tulo. Namondwe wamkulu anayamba pa nyanja, ndipo bwatolo linayamba kudzaza ndi madzi ndipo anali pa chiopsezo chachikulu.

Onani mutuwo Koperani




Luka 8:23
13 Mawu Ofanana  

moto ndi matalala, chipale chofewa ndi nkhungu; mphepo ya namondwe, yakuchita mau ake;


Galamukani, mugoneranji, Ambuye? Ukani, musatitaye chitayire.


Iwe wosautsidwa, wobelukabeluka ndi namondwe, wosatonthola mtima, taona, ndidzakhazika miyala yako m'mawangamawanga abwino, ndi kukhazika maziko ako ndi masafiro.


Ndipo panali, pakumkanikiza khamu la anthu, kudzamva mau a Mulungu, Iye analikuimirira m'mbali mwa nyanja ya Genesarete;


Ndipo panali limodzi la masiku aja, Iye analowa m'ngalawa, ndi ophunzira ake; nati kwa iwo, Tiolokere kutsidya lija la nyanja; ndipo anakankhiramo.


Ndipo m'mene tidalowa m'ngalawa ya ku Adramitio ikati ipite kunka ku malo a ku mbali ya Asiya, tinakankha, ndipo Aristariko Mmasedoniya wa ku Tesalonika, anali nafe.


Nanga ifenso tili m'moopsa bwanji nthawi zonse?


Pakuti sitili naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofooka zathu; koma wayesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa