Ndipo taonani, linandikhudza dzanja ndi kundikhalitsa ndi maondo anga, ndi zikhato za manja anga.
Mateyu 17:7 - Buku Lopatulika Ndipo Yesu anadza, nawakhudza nati, Ukani, musaopa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yesu anadza, nawakhudza nati, Ukani, musaopa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Yesu adabwera, naŵakhudza nkunena kuti, “Dzukani, musachite mantha.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yesu anabwera nawakhudza nati, “Dzukani, musaope.” |
Ndipo taonani, linandikhudza dzanja ndi kundikhalitsa ndi maondo anga, ndi zikhato za manja anga.
Ndipo m'mene analikulankhula ndi ine ndinagwidwa ndi tulo tatikulu, nkhope yanga pansi; koma anandikhudza, nandiimiritsa pokhala inepo.
inde pakunena ine m'kupemphera, munthu uja Gabriele, amene ndidamuona m'masomphenya poyamba paja, anauluka mwaliwiro nandikhudza ngati nthawi yakupereka nsembe ya madzulo.
ndipo m'mene anakhala ndi mantha naweramira pansi nkhope zao, anati kwa iwo, Mufuniranji wamoyo pa akufa?
Ndipo pamene ndinamuona Iye, ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa; ndipo anaika dzanja lake lamanja pa ine, nati, Usaope, Ine ndine Woyamba ndi Wotsiriza,