ndipo Iye anasandulika pamaso pao; ndipo nkhope yake inawala monga dzuwa, ndi zovala zake zinakhala zoyera mbuu monga kuwala.
Mateyu 17:1 - Buku Lopatulika Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wake, napita nao pa okha paphiri lalitali; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wake, napita nao pa okha pa phiri lalitali; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Patapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu adatenga Petro, Yakobe ndi Yohane, mbale wa Yakobeyo, nakwera nawo ku phiri lalitali, kwaokha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Patapita masiku asanu ndi limodzi Yesu anatenga Petro, Yakobo, ndi Yohane mʼbale wa Yakobo pa okha ndipo anakwera nawo pa phiri lalitali. |
ndipo Iye anasandulika pamaso pao; ndipo nkhope yake inawala monga dzuwa, ndi zovala zake zinakhala zoyera mbuu monga kuwala.
Ndipo anatenga Petro ndi ana awiri a Zebedeo pamodzi naye, nayamba kugwidwa ndi chisoni ndi kuthedwa nzeru.
Ndipo pamene anakhala Iye paphiri la Azitona, popenyana ndi Kachisi, anamfunsa Iye m'tseri Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Andrea, kuti,
Ndipo sanalole munthu yense kutsagana naye, koma Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wake wa Yakobo.
Ndipo pakufika Iye kunyumbako, sanaloleze wina kulowa naye pamodzi, koma Petro, ndi Yohane, ndi Yakobo, ndi atate wa mwanayo, ndi amake.
Nthawi yachitatu iyi ndilinkudza kwa inu. Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu maneno onse adzakhazikika.
Pakuti sitinatsate miyambi yachabe, pamene tinakudziwitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Khristu, koma tinapenya m'maso ukulu wake.
ndipo mau awa ochokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi Iye m'phiri lopatulika lija.