Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 13:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo pamene anakhala Iye paphiri la Azitona, popenyana ndi Kachisi, anamfunsa Iye m'tseri Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Andrea, kuti,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo pamene anakhala Iye pa phiri la Azitona, popenyana ndi Kachisi, anamfunsa Iye m'tseri Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Andrea, kuti,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Pambuyo pake Yesu adakhala pansi, pa Phiri la Olivi, kuyang'anana ndi Nyumba ya Mulungu. Tsono Petro, Yakobe, Yohane ndi Andrea adamufunsa paokha, kuti,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Yesu atakhala pansi pa phiri la Olivi moyangʼanana ndi Nyumba ya Mulungu, Petro, Yakobo, Yohane ndi Andreya anamufunsa Iye pambali kuti,

Onani mutuwo Koperani




Marko 13:3
13 Mawu Ofanana  

Ndipo ophunzirawo anadza, nati kwa Iye, Chifukwa chanji muphiphiritsira iwo m'mafanizo?


Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m'nyumba; ndimo ophunzira ake anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m'munda.


Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wake, napita nao pa okha paphiri lalitali;


Ndipo pamene iwo anayandikira ku Yerusalemu, nafika ku Betefage, kuphiri la Azitona, pamenepo Yesu anatumiza ophunzira awiri,


Ndipo pamene Iye analikukhala pansi paphiri la Azitona, ophunzira anadza kwa Iye pa yekha, nanena, Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthawi ya pansi pano?


Ndipo anadza kwa Iye Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedeo, nanena naye, Mphunzitsi, tifuna kuti mudzatichitire chimene chilichonse tidzapempha kwa Inu.


Tiuzeni, zinthu izi zidzachitika liti? Ndi chotani chizindikiro chake chakuti zili pafupi pa kumalizidwa zinthu izi zonse?


Ndipo anatenga pamodzi ndi Iye Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nayamba kudabwa kwambiri, ndi kusauka mtima ndithu.


ndipo sanalankhule nao wopanda fanizo: koma m'tseri anatanthauzira zonse kwa ophunzira ake.


Ndipo sanalole munthu yense kutsagana naye, koma Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wake wa Yakobo.


Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nakwera nao paphiri lalitali padera pa okha; ndipo anasandulika pamaso pao:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa