Mateyu 15:12 - Buku Lopatulika Pomwepo anadza ophunzira, nanena kwa Iye, Mudziwa kodi kuti Afarisi anakhumudwa pakumva chonenacho? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo anadza ophunzira, nanena kwa Iye, Mudziwa kodi kuti Afarisi anakhumudwa pakumva chonenacho? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo ophunzira ake adadzamufunsa kuti, “Kodi mukudziŵa kuti Afarisi aja akhumudwa atamva zija mwanenazi?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo ophunzira anabwera kwa Iye ndipo anamufunsa kuti, “Kodi mukudziwa kuti Afarisi anakhumudwa pamene anamva mawu aja?” |
si chimene chilowa m'kamwa mwake chiipitsa munthu; koma chimene chituluka m'kamwa mwake, ndicho chiipitsa munthu.
Koma Iye anayankha nati, Mmera wonse, umene Atate wanga wa Kumwamba sanaubzale, udzazulidwa.
Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pake udzapezamo rupiya; tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamutu pa iwe ndi Ine.
Koma sitidawafumukire mowagonjera ngakhale ora limodzi; kuti choonadi cha Uthenga Wabwino chikhalebe ndi inu.
Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso.