Mateyu 17:27 - Buku Lopatulika27 Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pake udzapezamo rupiya; tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamutu pa iwe ndi Ine. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201427 Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pake udzapezamo rupiya; tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamtu pa iwe ndi Ine. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa27 Koma kuwopa kuŵakhumudwitsa a ku Nyumba ya Mulunguŵa, kaŵedze nsomba ku nyanja. Nsomba imene ukayambire kuŵedza, ukaikanule kukamwa, ndipo ukapezamo ndalama. Ukatenge ndalamayo nkukakhomera msonkho wanga ndi wako womwe.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero27 Koma kuti ife tisawakhumudwitse pita ku nyanja kaponye mbedza yako. Katenge nsomba imene ukayambe kuyikola; kayitsekule kukamwa ndipo ukapezamo ndalama. Katenge ndalamayo ndi kukapereka msonkho wanga ndi wanu. Onani mutuwo |