Mateyu 13:9 - Buku Lopatulika Amene ali ndi makutu, amve. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Amene ali ndi makutu, amve. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yesu adati, “Amene ali ndi makutu, amve!” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amene ali ndi makutu amve.” |
Ndipo ophunzirawo anadza, nati kwa Iye, Chifukwa chanji muphiphiritsira iwo m'mafanizo?
Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Iye amene apambana sadzachitidwa choipa ndi imfa yachiwiri.
Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wopambana, ndidzampatsa mana obisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pamwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu aliyense koma iye wakuulandira.
Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye amene apambana ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli mu Paradaiso wa Mulungu.