Mateyu 12:12 - Buku Lopatulika Nanga kuposa kwake kwa munthu ndi nkhosa nkotani! Chifukwa cha ichi nkuloleka kuchita zabwino tsiku la Sabata. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nanga kuposa kwake kwa munthu ndi nkhosa nkotani! Chifukwa cha ichi nkuloleka kuchita zabwino tsiku la Sabata. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nanji munthu, amene amaposa nkhosa kutalitali! Ndiye kutitu Malamulo amalola kuchita zabwino pa tsiku la Sabata.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nanga munthu sali oposa nkhosa kwambiri! Chifukwa chake nʼkololedwa kuchita zabwino pa Sabata.” |
Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?
Ndipo ananena kwa iwo, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchita zabwino, kapena zoipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha? Koma anakhala chete.
Lingirirani makwangwala, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!
Ndipo panali pamene Iye analowa m'nyumba ya mmodzi wa akulu a Afarisi tsiku la Sabata, kukadya, iwo analikumzonda Iye.
Ndipo Iye ananyamuka, naimirira. Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ndikufunsani inu, Kodi nkulola tsiku la Sabata, kuchita zabwino, kapena kuchita zoipa? Kupulumutsa moyo, kapena kuuononga?