Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 14:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo panali pamene Iye analowa m'nyumba ya mmodzi wa akulu a Afarisi tsiku la Sabata, kukadya, iwo analikumzonda Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo panali pamene Iye analowa m'nyumba ya mmodzi wa akulu a Afarisi tsiku la Sabata, kukadya, iwo analikumzonda Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pa tsiku lina la Sabata Yesu adakadya kwa mkulu wina wa m'gulu la Afarisi, ndipo Afarisi anzake ankamupenyetsetsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Pa tsiku lina la Sabata, Yesu atapita kukadya ku nyumba ya Mfarisi wodziwika, Afarisi anamulonda mosamalitsa.

Onani mutuwo Koperani




Luka 14:1
19 Mawu Ofanana  

Woipa aunguza wolungama, nafuna kumupha.


Ndipo akadza kundiona wina angonena bodza; mumtima mwake adzisonkhera zopanda pake, akanka nayenda namakanena.


Komatu amkhalira upo kuti amkankhire pansi ulemu wake; akondwera nao mabodza; adalitsa ndi m'kamwa mwao, koma atemberera mumtima.


Pakuti monga asinkha m'kati mwake, ali wotere; ati kwa iwe, Idya numwe; koma mtima wake suli pa iwe.


Nanga kuposa kwake kwa munthu ndi nkhosa nkotani! Chifukwa cha ichi nkuloleka kuchita zabwino tsiku la Sabata.


Ndipo anamuyang'anira Iye, ngati adzamchiritsa tsiku la Sabata; kuti ammange mlandu.


Ndipo pakulankhula Iye, anamuitana Mfarisi kuti adye naye; ndipo analowa naseama kudya.


Ndipo onani, panali pamaso pake munthu wambulu.


Ndipo pamene Afarisi anamfunsa Iye, kuti, Ufumu wa Mulungu ukudza liti, anawayankha, nati, Ufumu wa Mulungu sukudza ndi maonekedwe;


Ndipo anamyang'anira, natumiza ozonda, amene anadzionetsera ngati olungama mtima, kuti akamkole pa mau ake, kotero kuti akampereke Iye ku ukulu ndi ulamuliro wa kazembe.


Ndipo alembi ndi Afarisi analikumzonda Iye, ngati adzachiritsa tsiku la Sabata; kuti akapeze chomneneza Iye.


Koma panali munthu wa Afarisi, dzina lake Nikodemo, mkulu wa Ayuda.


Koma ananyamukapo wina pabwalo la akulu a milandu, ndiye Mfarisi, dzina lake Gamaliele, mphunzitsi wa malamulo, wochitidwa ulemu ndi anthu onse, nalamula kuti atumwiwo akhale kunja pang'ono.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa