Mateyu 10:11 - Buku Lopatulika Ndipo m'mzinda uliwonse, kapena m'mudzi, mukalowamo, mufunsitse amene ali woyenera momwemo; ndipo bakhalani komweko kufikira mutulukamo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'mzinda uliwonse, kapena m'mudzi. Mukalowamo, mufunsitse amene ali woyenera momwemo; ndipo bakhalani komweko kufikira mutulukamo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Pamene mwaloŵa mu mzinda kapena m'mudzi uliwonse, mufunsitse za munthu wofunadi kukulandirani. Mukakhale kunyumba kwake mpaka nthaŵi yochoka. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mukalowa mu mzinda ndi mʼmudzi uliwonse, funafunani munthu woyenera ndipo mukhale mʼnyumba mwake kufikira mutachoka. |
kapena thumba la kamba la kunjira, kapena malaya awiri, kapena nsapato, kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira zakudya zake.
Ndipo ananena nao, Kumene kulikonse mukalowa m'nyumba, khalani komweko kufikira mukachokako.
Ndipo m'mene anachiona anadandaula onse, nanena, Analowa amchereze munthu ali wochimwa.
Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pake anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m'nyumba yanga, mugone m'menemo. Ndipo anatiumiriza ife.