Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 10:10 - Buku Lopatulika

10 kapena thumba la kamba la kunjira, kapena malaya awiri, kapena nsapato, kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira zakudya zake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 kapena thumba la kamba la kunjira, kapena malaya awiri, kapena nsapato, kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira zakudya zake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Musatenge thumba lapaulendo, kapena mikanjo iŵiri, kapena nsapato, kapena ndodo. Paja wantchito ngwoyenera kulandira zosoŵa zake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 musatenge thumba la paulendo, kapena malaya awiri kapena nsapato kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira chakudya chake.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 10:10
12 Mawu Ofanana  

Ndipo muzidye pamalo ponse, inu ndi a pabanja panu; popeza ndizo mphotho yanu mwa ntchito yanu m'chihema chokomanako.


Ndipo m'mzinda uliwonse, kapena m'mudzi, mukalowamo, mufunsitse amene ali woyenera momwemo; ndipo bakhalani komweko kufikira mutulukamo.


ndipo anawauza kuti asatenge kanthu ka paulendo, koma ndodo yokha; asatenge mkate, kapena thumba, kapena ndalama m'lamba lao;


Koma iye anayankha nanena kwa iwo, Iye amene ali nao malaya awiri apatse kwa iye amene alibe; ndi iye amene ali nazo zakudya achite chomwecho.


Ndipo Iye anati kwa iwo, Musanyamule kanthu ka paulendo, kapena ndodo, kapena thumba, kapena mkate, kapena ndalama; ndipo musakhale nao malaya awiri.


Chofunda chija ndinachisiya ku Troasi kwa Karpo, udze nacho pakudza iwe, ndi mabuku, makamaka zikopa zija zolembedwa.


Natenga ndodo yake m'dzanja lake nadzisankhira miyala isanu yosalala ya mumtsinje, naiika m'thumba la kubusa, limene anali nalo ndilo chibete; ndi choponyera miyala chinali m'dzanja lake, momwemo anayandikira kwa Mfilistiyo.


Ndipo Saulo ananena ndi mnyamata wake, Koma taona, tikapitako timtengere chiyani munthuyo? Popeza mkate udatha m'zotengera zathu, ndiponso tilibe mphatso yakumtengera munthu wa Mulungu, tili nacho chiyani?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa