ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.
Mateyu 1:18 - Buku Lopatulika Ndipo kubadwa kwake kwa Yesu Khristu kunali kotere: Amai wake Maria anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kubadwa kwake kwa Yesu Khristu kunali kotere: Amai wake Maria anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iye ali ndi pakati mwa Mzimu Woyera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kubadwa kwa Yesu Khristu kudaatere: amai ake Maria adaafunsidwa mbeta ndi Yosefe; koma asanaloŵane, Maria adaapezeka kuti ali ndi pathupi mwa mphamvu za Mzimu Woyera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kubadwa kwa Yesu Khristu kunali motere: Amayi ake, Mariya, anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanagone malo amodzi, anapezeka ali woyembekezera mwana mwa mphamvu ya Mzimu Woyera. |
ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitendeni chake.
Pamene Iye anali chilankhulire ndi makamu, onani, amake ndi abale ake anaima panja, nafuna kulankhula naye.
Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Maria amake, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golide ndi lubani ndi mure.
Ambuye wandichitira chotero m'masiku omwe Iye anandipenyera, kuchotsa manyazi anga pakati pa anthu.
kukalembedwa iye mwini pamodzi ndi Maria, wopalidwa naye ubwenzi; ndi uyu anali ndi pakati.
Pakakhala namwali, wosadziwa mwamuna, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, ndipo anampeza m'mzinda mwamuna, nagona naye;
Mwa ichi polowa m'dziko lapansi, anena, Nsembe ndi chopereka simunazifune, koma thupi munandikonzera Ine.
Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa, wakukhala wopitirira miyamba;