Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Masalimo 99:4 - Buku Lopatulika

Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda chiweruzo; Inu mukhazikitsa zolunjika, muchita chiweruzo ndi chilungamo mu Yakobo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda chiweruzo; Inu mukhazikitsa zolunjika, muchita chiweruzo ndi chilungamo m'Yakobo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ndinu Mfumu yamphamvu, yokonda chilungamo, mwakhazikitsa khalidwe losakondera ndiponso kuweruza kolungama m'dziko la Yakobe.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mfumu yamphamvu, iyo imakonda chilungamo Inu mwakhazikitsa khalidwe losakondera; mwachita zolungama ndi zoyenera mwa Yakobo.

Onani mutuwo



Masalimo 99:4
17 Mawu Ofanana  

Kunena za Wamphamvuyonse, sitingamsanthule; ndiye wa mphamvu yoposa; koma mwa chiweruzo ndi chilungamo chochuluka samasautsa.


Pakuti Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama; woongoka mtima adzapenya nkhope yake.


Pamaso pa Yehova, popeza akudza kudzaweruza dziko lapansi; adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndipo mitundu ya anthu molunjika.


Iye sadzalephera kapena kudololoka, kufikira atakhazikitsa chiweruzo m'dziko lapansi; ndipo zisumbu zidzalindira chilamulo chake.


Pakuti monga dziko liphukitsa mphundu zake, ndi monga munda umeretsa zobzalamo, momwemo Ambuye Yehova adzaphukitsa chilungamo ndi matamando pamaso pa amitundu onse.


Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.


Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzamuukitsira Davide Mphukira wolungama, ndipo Iye adzakhala Mfumu, adzachita mwanzeru, nadzachita chiweruzo ndi chilungamo m'dziko lino.


Aweruzira ana amasiye ndi mkazi wamasiye; ndipo akonda mlendo, ndi kumpatsa chakudya ndi chovala.


kudzachitira onse chiweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pa ntchito zao zonse zosapembedza, ndi pa zolimba zimene ochimwa osapembedza adalankhula pa Iye.


Ndipo ndinaona mutatseguka mu Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi Iye wakumkwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nachita nkhondo molungama.


Ndipo ali nalo pa chovala chake ndi pa ntchafu yake dzina lolembedwa, MFUMU YA MAFUMU, NDI MBUYE WA AMBUYE.