Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 23:5 - Buku Lopatulika

5 Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzamuukitsira Davide Mphukira wolungama, ndipo Iye adzakhala Mfumu, adzachita mwanzeru, nadzachita chiweruzo ndi chilungamo m'dziko lino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzamuukitsira Davide Mphukira wolungama, ndipo Iye adzakhala Mfumu, adzachita mwanzeru, nadzachita chiweruzo ndi chilungamo m'dziko lino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Chauta akunena kuti, “Akubwera masiku pamene ndidzaphukitsira Davide nthambi yoongoka imene idzakhala mfumu yanzeru ndi yoweruza m'dzikomo mwachilungamo ndi mosakondera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Yehova akuti, “Masiku akubwera, pamene ndidzaphukitsira Davide Nthambi yowongoka. Imeneyi ndiye mfumu imene idzalamulira mwanzeru, mwachilungamo ndi mosakondera mʼdziko.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 23:5
49 Mawu Ofanana  

Mulungu wa Israele anati, Thanthwe la Israele linalankhula ndi ine; kudzakhala woweruza anthu molungama; woweruza m'kuopa Mulungu.


Ndipo pindulani, mu ukulu wanu yendani, kaamba ka choonadi ndi chifatso ndi chilungamo; ndipo dzanja lanu lidzakuphunzitsani zoopsa.


ndi tsinde limene dzanja lanu lamanja linaoka, ndi mphanda munadzilimbikitsira.


Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda chiweruzo; Inu mukhazikitsa zolunjika, muchita chiweruzo ndi chilungamo mu Yakobo.


Yehova wakwezedwa; pakuti akhala kumwamba; Iye wadzaza Ziyoni ndi chiweruzo ndi chilungamo.


Tsiku limenelo mphukira ya Yehova idzakhala yokongola ndi ya ulemerero, chipatso cha nthaka chidzakhala chokometsetsa ndi chokongola, kwa iwo amene adzapulumuka a Israele.


Ine Yehova ndakuitana Iwe m'chilungamo, ndipo ndidzagwira dzanja lako ndi kusunga Iwe, ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, ndi kuunika kwa amitundu;


Koma mwa Yehova yekha, wina adzati kwa Ine, muli chilungamo ndi mphamvu; ngakhale kwa Iyeyo anthu adzafika, ndi onse amene anamkwiyira, adzakhala ndi manyazi.


Taonani, Mtumiki wanga adzachita mwanzeru; adzakwezedwa ndi kutukulidwa pamwamba, nadzakhala pamwambamwamba.


Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, Iye adzaona mbeu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m'manja mwake.


Pakuti ameneyo adzaphuka pamaso pake ngati mtengo wanthete, ndi ngati muzu womera m'nthaka youma; Iye alibe maonekedwe, pena kukongola; ndipo pamene timuona palibe kukongola kuti timkhumbe.


Pakuti zida zonse za mwamuna wovala zida za nkhondo m'phokosomo, ndi zovala zomvimvinika m'mwazi, zidzakhala zonyeka ngati nkhuni.


Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.


Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.


Kodi udzakhala mfumu, chifukwa iwe uyesa kuposa ena ndi mikungudza? Kodi atate wako sanadye ndi kumwa, ndi kuweruza molungama? Kumeneko kunamkomera.


Yehova atero: Chitani chiweruzo ndi chilungamo, landitsani ofunkhidwa m'dzanja la wosautsa; musachite choipa, musamchitire mlendo chiwawa, kapena ana amasiye, kapena akazi amasiye, musakhetse mwazi wosachimwa pamalo pano.


Atero Yehova, Lembani munthu uyu wopanda ana, munthu wosaona phindu masiku ake; pakuti palibe munthu wa mbeu zake adzaona phindu, ndi kukhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi kulamuliranso mu Yuda.


Masiku ake Yuda adzapulumutsidwa, ndipo Israele adzakhala mokhazikika, dzina lake adzatchedwa nalo, ndilo Yehova ndiye chilungamo chathu.


Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.


Pakuti, taona, masiku adzadza, ati Yehova, amene ndidzabwezanso undende wa anthu anga Aisraele ndi Ayuda, ati Yehova; ndipo ndidzawabwezera kudziko limene ndinapatsa makolo ao. Ndipo adzakhala nalo.


koma adzamtumikira Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, imene Ndidzawaukitsira.


Taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzafesera nyumba ya Israele ndi nyumba ya Yuda ndi mbeu ya anthu ndi mbeu ya nyama.


Ndidzagubuduzagubuduza ufumu uno, sudzakhalanso kufikira akadza Iye mwini chiweruzo; ndipo ndidzaupereka kwa Iye.


Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopirikitsidwa, ndi kulukira chika yothyoka mwendo, ndikulimbitsa yodwalayo; koma yonenepa ndi yolimba ndidzaziononga, ndidzazidyetsa ndi chiweruzo.


Ndipo ndidzawautsira mbeu yomveka, ndipo sadzachotsedwanso ndi njala m'dzikomo, kapena kusenzanso manyazi a amitundu.


M'dzikomo ili lidzakhala lakelake mu Israele; ndipo akalonga anga sadzazunzanso anthu anga, koma adzapereka dziko kwa nyumba ya Israele monga mwa mafuko ao.


Masabata makumi asanu ndi awiri alamulidwira anthu a mtundu wako ndi mzinda wako wopatulika, kumaliza cholakwacho, ndi kutsiriza machimo, ndi kutetezera mphulupulu, ndi kufikitsa chilungamo chosalekeza, ndi kukhomera chizindikiro masomphenya ndi zonenera, ndi kudzoza malo opatulika kwambiri.


Ndipo ana a Yuda ndi ana a Israele adzasonkhanidwa pamodzi, nadzadziikira mkulu mmodzi, nadzakwera kuchoka m'dziko; pakuti tsiku la Yezireele ndi lalikulu.


atatero ana a Israele adzabwera, nadzafuna Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, nadzafika ndi mantha kwa Yehova, ndi ku ukoma wake masiku otsiriza.


Tsiku lomwelo ndidzautsa msasa wa Davide udagwawo, ndi kukonzanso zopasuka zake; ndipo ndidzautsa zogumuka zake, ndi kuumanga monga masiku a kalelo;


Chifukwa chake Iye adzawapereka kufikira nthawi yoti wobalayo wabala; pamenepo otsala a abale ake adzabwera pamodzi ndi ana a Israele.


Tamvera tsono, Yoswa mkulu wa ansembe, iwe ndi anzako akukhala pansi pamaso pako; pakuti iwo ndiwo chizindikiro; pakuti taonani, ndidzafikitsa mtumiki wanga, ndiye Mphukira.


Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.


nati, Ali kuti amene anabadwa mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kum'mawa, ndipo tinadzera kudzamlambira Iye.


Filipo anapeza Natanaele, nanena naye, Iye amene Mose analembera za Iye m'chilamulo, ndi aneneri, tampeza, ndiye Yesu mwana wa Yosefe wa ku Nazarete.


Natanaele anayankha Iye, Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu mfumu ya Israele.


Koma kwa Iye muli inu mwa Khristu Yesu, amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi chilungamo ndi chiyeretso ndi chiombolo;


Pakuti powatchulira iwo chifukwa, anena, Taonani, akudza masiku, anena Ambuye, Ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israele, ndi nyumba ya Yuda,


Ndipo ndinaona mutatseguka mu Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi Iye wakumkwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nachita nkhondo molungama.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa