Masalimo 9:7 - Buku Lopatulika Koma Yehova akhala chikhalire, anakonzeratu mpando wachifumu wake kuti aweruze. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Yehova akhala chikhalire, anakonzeratu mpando wachifumu wake kuti aweruze. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma Chauta amakhala pa mpando wake waufumu nthaŵi zonse, adakhazika mpando wake kuti aziweruza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova akulamulira kwamuyaya; wakhazikitsa mpando wake waufumu woweruzira. |
Yehova anakhazika mpando wachifumu wake Kumwamba; ndi ufumu wake uchita mphamvu ponsepo.
Chilungamo ndi chiweruzo ndiwo maziko a mpando wanu wachifumu; chifundo ndi choonadi zitsogolera pankhope panu.
Asanabadwe mapiri, kapena musanalenge dziko lapansi, ndi lokhalamo anthu, inde, kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha, Inu ndinu Mulungu.
Koma ichi chimodzi musaiwale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka chikwi, ndi zaka chikwi ngati tsiku limodzi.
Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwe malo ao.