Ndipo ndidzalimbitsa pangano langa ndi Ine ndi iwe pa mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao, kuti likhale pangano la nthawi zonse, kuti ndikhale Mulungu wako ndi wa mbeu zako za pambuyo pako.
Masalimo 67:6 - Buku Lopatulika Dziko lapansi lapereka zipatso zake, Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Dziko lapansi lapereka zipatso zake, Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaka yabereka zipatso zake, Mulungu, Mulungu wathu watidalitsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthaka yabereka zokolola zake; tidalitseni Mulungu wathu. |
Ndipo ndidzalimbitsa pangano langa ndi Ine ndi iwe pa mbeu zako za pambuyo pako m'mibadwo yao, kuti likhale pangano la nthawi zonse, kuti ndikhale Mulungu wako ndi wa mbeu zako za pambuyo pako.
Pakuti Mulungu ameneyo ndiye Mulungu wathu kunthawi za nthawi, adzatitsogolera kufikira imfa.
Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israele, Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili ndi dzina langa nthawi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m'mibadwomibadwo.
Nthawi yomweyo, ati Yehova, ndidzakhala Mulungu wa mabanja onse a Israele, ndipo iwo adzakhala anthu anga.
Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israele atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika chilamulo changa m'kati mwao, ndipo m'mtima mwao ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga;
Dziko lidzaperekanso zipatso zake, ndipo mudzadya ndi kukhuta, ndi kukhalamo okhazikika.
ndidzakupatsani mvula m'nyengo zake, ndi dziko lidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m'minda idzabala zipatso zake.