Nadzipatula a mbumba ya Israele kwa alendo onse, naimirira, nawulula zochimwa zao, ndi mphulupulu za makolo ao.
Masalimo 51:3 - Buku Lopatulika Chifukwa ndazindikira machimo anga; ndipo choipa changa chili pamaso panga chikhalire. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa ndazindikira machimo anga; ndipo choipa changa chili pamaso panga chikhalire. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zolakwa zanga ndikuzidziŵa, kuchimwa kwanga ndikukuzindikira nthaŵi zonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti ndikudziwa mphulupulu zanga, ndipo tchimo langa lili pamaso panga nthawi zonse. |
Nadzipatula a mbumba ya Israele kwa alendo onse, naimirira, nawulula zochimwa zao, ndi mphulupulu za makolo ao.
Apenyerera anthu, ndi kuti, ndinachimwa, ndaipsa choongokacho, ndipo sindinapindule nako.
Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibise. Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.
Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima.
Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira machimo ako.
Pakuti zolakwa zathu zachuluka pamaso pa Inu, ndipo machimo athu atineneza ife; pakuti zolakwa zathu zili ndi ife, ndipo zoipa zathu tizidziwa;
Tigone m'manyazi athu, kunyala kwathu kutifunde ife; pakuti tamchimwira Yehova Mulungu wathu, ife ndi makolo athu, kuyambira ubwana wathu kufikira lero lomwe; ndipo sitidamvere mau a Yehova Mulungu wathu.