Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri, mantha andizinga. Pondipangira chiwembu, anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga.
Masalimo 41:7 - Buku Lopatulika Onse akudana nane andinong'onezerana; apangana chondiipsa ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Onse akudana nane andinong'onezerana; apangana chondiipsa ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Onse odana nane amanong'onezana za ine, amayesa kuti zoipa zandigwera chifukwa cha kuipa kwanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Adani anga onse amanongʼonezana pamodzi kulimbana nane, iwo amalingalira zoyipa kwambiri za ine, ponena kuti, |
Pakuti ndamva ugogodi wa ambiri, mantha andizinga. Pondipangira chiwembu, anatsimikiza mtima kulanda moyo wanga.
anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani;
Pakuti ndiopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuna; kuti kaya pangakhale chotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi, ukazitape, zodzikuza, mapokoso;