Masalimo 32:9 - Buku Lopatulika Musakhale monga kavalo, kapena ngati bulu, wopanda nzeru; zomangira zao ndizo cham'kamwa ndi chapamutu zakuwakokera, pakuti ukapanda kutero sadzakuyandikiza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Musakhale monga kavalo, kapena ngati bulu, wopanda nzeru; zomangira zao ndizo cham'kamwa ndi chapamutu zakuwakokera, pakuti ukapanda kutero sadzakuyandikiza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Musakhale opanda nzeru ngati kavalo kapena bulu amene ayenera kumuwongolera ndi chitsulo cham'kamwa ndi chapamutu, chifukwa ukapanda kutero, nyamazo sizidzakumvera.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Usakhale ngati kavalo kapena bulu, zimene zilibe nzeru, koma ziyenera kuwongoleredwa ndi zitsulo za mʼkamwa ndi pamutu, ukapanda kutero sizibwera kwa iwe. |
wakutilangiza ife koposa nyama za padziko, wakutipatsa nzeru zoposa mbalame za m'mlengalenga?
Chikoti chiyenera kavalo, ndi cham'kamwa chiyenera bulu, ndi nthyole iyenera pamsana pa zitsiru.
Kumva ndamva Efuremu alinkulirira kotero, Mwandilanga ine, ndipo ndalangidwa, monga mwanawang'ombe wosazolowera goli; munditembenuze ine, ndipo ine ndidzatembenuka; pakuti inu ndinu Yehova Mulungu wanga.
Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ochenjera kuchita choipa koma kuchita chabwino sakudziwa.
Koma ngati tiikira akavalo zogwirira m'kamwa mwao atimvere, tipotolozanso thupi lao lonse.