Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yakobo 3:3 - Buku Lopatulika

3 Koma ngati tiikira akavalo zogwirira m'kamwa mwao atimvere, tipotolozanso thupi lao lonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Koma ngati tiikira akavalo zogwirira m'kamwa mwao atimvere, tipotolozanso thupi lao lonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Timaika kachitsulo m'kamwa mwa kavalo kuti atimvere, ndipo tingathe kumaongolera thupi lake lonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Tikayika tizitsulo mʼkamwa mwa akavalo kuti atimvere, timatha kuwongolera thupi lake lonse.

Onani mutuwo Koperani




Yakobo 3:3
7 Mawu Ofanana  

Chifukwa cha kundizazira kwako, ndi popeza kudzikuza kwako kwandifikira m'makutu mwanga, ndidzakukowa ndi ngowe yanga m'mphuno mwako, ndi cham'kamwa changa m'milomo mwako; ndipo ndidzakubwezera panjira unadzerayi.


Ndani adzasenda chovala chake chakunja? Adzalowa ndani kumizere iwiri ya mano ake?


Musakhale monga kavalo, kapena ngati bulu, wopanda nzeru; zomangira zao ndizo cham'kamwa ndi chapamutu zakuwakokera, pakuti ukapanda kutero sadzakuyandikiza.


Ndinati, Ndidzasunga njira zanga, kuti ndingachimwe ndi lilime langa. Ndidzasunga pakamwa panga ndi cham'kamwa, pokhala woipa ali pamaso panga.


Chifukwa cha kundikwiyira Ine kwako, ndi popeza kudzikweza kwako kwafika m'makutu mwanga. Ine ndidzaika mbedza yanga m'mphuno mwako, ndi chapakamwa changa m'milomo yako, ndipo ndidzakubweza iwe m'njira yomwe unadzerayo.


Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.


Taonani, zombonso, zingakhale zazikulu zotere, nkutengedwa ndi mphepo zolimba, zipotozeka ndi tsigiro laling'ono ndithu kumene kulikonse afuna wogwira tsigiro.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa