Masalimo 148:6 - Buku Lopatulika Anazikhazikanso kunthawi za nthawi; anazipatsa chilamulo chosatumphika. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anazikhazikanso kunthawi za nthawi; anazipatsa chilamulo chosatumphika. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adazikhazikitsa kuti zikhale mpaka muyaya, adaikapo lamulo limene silingathe kusinthika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anaziyika pa malo ake ku nthawi za nthawi; analamula ndipo sizidzatha. |
Yehova achita ufumu; wadziveka ndi ukulu; wadziveka Yehova, wadzimangirira mphamvu m'chuuno; dziko lomwe lokhalamo anthu likhakizika, silidzagwedezeka.
Pakuti kumeneku kuli kwa Ine monga madzi a Nowa; pakuti monga ndinalumbira kuti madzi a Nowa sadzamizanso padziko lapansi, momwemo ndinalumbira kuti sindidzakukwiyira iwe, pena kukudzudzula.
Yehova atero: Likaleka kukhala pangano langa la usana ndi usiku, ngati sindinalemba malemba a kumwamba ndi dziko lapansi;