Aleluya; Ulemekeze Yehova, moyo wanga.
Tamandani Chauta! Tamanda Chauta, iwe mtima wanga.
Tamandani Yehova. Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
Lemekeza Yehova, moyo wanga; ndi zonse za m'kati mwanga zilemekeze dzina lake loyera.
Lemekezani Yehova, inu, ntchito zake zonse, ponseponse pali ufumu wake: Lemekeza Yehova, moyo wanga iwe.
Ochimwa athedwe kudziko lapansi, ndi oipa asakhalenso. Yamika Yehova, moyo wanga. Aleluya.
Kuti asamalire malemba ake, nasunge malamulo ake. Aleluya.