Kunena za mutu wao wa iwo akundizinga, choipa cha milomo yao chiwaphimbe.
Adani anga ondizinga asandigonjetse. Mau ao otemberera aŵabwerere.
Mitu ya amene andizungulira iphimbidwe ndi masautso amene milomo yawo yayambitsa.
Pamenepo Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse ananena naye, Apange mtengo, msinkhu wake mikono makumi asanu, ndi mawa mukanene nayo mfumu kuti ampachike Mordekai pamenepo; nimulowe pamodzi ndi mfumu kumadyerero wokondwera. Ndipo ichi chidakomera Hamani, napangitsa anthu mtengowo.
Nampachika Hamani pa mtengo adaukonzera Mordekai. Pamenepo mkwiyo wa mfumu unatsika.
Adzawakhumudwitsa, lilime lao lidzawatsutsa; onse akuwaona adzawathawa.
Chovuta chake chidzambwerera mwini, ndi chiwawa chake chidzamgwera pakati pamutu pake.
Ndipo anawabwezera zopanda pake zao, nadzawaononga m'choipa chao; Yehova Mulungu wathu adzawaononga.
M'kamwa mwa wolungama ndi kasupe wa moyo; koma m'kamwa mwa oipa mubisa chiwawa.
Madalitso ali pamutu pa wolungama; koma m'kamwa mwa oipa mubisa chiwawa.
M'kulakwa kwa milomo muli msampha woipa; koma wolungama amatuluka m'mavuto.
M'kamwa mwa wopusa mumuononga, milomo yake ikhala msampha wa moyo wake.
Ndipo anthu onse anavomereza, ndi kuti, Mwazi wake uli pa ife ndi pa ana athu.
Ndikadapanda kuopa mkwiyo wa pa mdani, angayese molakwa outsana nao, anganene, Lakwezeka dzanja lathu, ndipo Yehova sanachite ichi chonse.