Masalimo 139:9 - Buku Lopatulika Ndikadzitengera mapiko a mbandakucha, ndi kukhala ku malekezero a nyanja; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndikadzitengera mapiko a mbandakucha, ndi kukhala ku malekezero a nyanja; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikaulukira kotulukira dzuŵa, kapena kukafika kuzambwe, ku mathero a nyanja, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati ndiwulukira kotulukira dzuwa, ngati ndikakhala ku malekezero a nyanja, |
Kutuluka kwake lituluka kolekezera thambo, ndipo kuzungulira kwake lifikira ku malekezero ake; ndipo kulibe kanthu kobisalira kutentha kwake.
Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m'mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati anaang'ombe onenepa otuluka m'khola.