Masalimo 12:8 - Buku Lopatulika Oipa amayenda mozungulirazungulira, potamanda iwo chonyansa mwa ana a anthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Oipa amayenda mozungulirazungulira, potamanda iwo chonyansa mwa ana a anthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa pakuti anthu oipa amangoyendayenda ponseponse, ndipo anzao amayamikira zochita zao zoipa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Oyipa amangoyendayenda ponseponse anthu akamayamikira zochita zawo. |
Ndi m'malo mwake adzauka munthu woluluka, amene anthu sanampatse ulemu wa ufumu, koma adzafika kachetechete, nadzalanda ufumu ndi mau osyasyalika.
Pakuti asunga malemba a Omuri, ndi ntchito za nyumba ya Ahabu, ndipo mumayenda mu uphungu wao; kuti ndikusandulize bwinja, ndi okhalamo chotsonya; ndipo mudzasenza chitonzo cha anthu anga.