Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 11:21 - Buku Lopatulika

21 Ndi m'malo mwake adzauka munthu woluluka, amene anthu sanampatse ulemu wa ufumu, koma adzafika kachetechete, nadzalanda ufumu ndi mau osyasyalika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndi m'malo mwake adzauka munthu woluluka, amene anthu sanampatse ulemu wa ufumu, koma adzafika kachetechete, nadzalanda ufumu ndi mau osyasyalika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 “Mʼmalo mwake mudzalowa munthu wonyozeka amene si wa banja laufumu. Iye adzabwera pamene anthu akuganiza kuti ali pa mtendere, ndipo adzalanda ufumuwo mwa chinyengo.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 11:21
17 Mawu Ofanana  

Oipa amayenda mozungulirazungulira, potamanda iwo chonyansa mwa ana a anthu.


M'maso mwake munthu woonongeka anyozeka; koma awachitira ulemu akuopa Yehova. Atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ai.


Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.


Wopusa sadzayesedwanso woolowa manja, ngakhale wouma manja sadzayesedwa mfulu.


Ndipo m'malo mwake adzauka wina wakupititsa wamsonkho pa ulemerero wa ufumuwo; koma atatha masiku owerengeka adzathyoledwa iye, si mwamkwiyo, kapena kunkhondo ai.


Ndipo akuchitira choipa chipanganocho iye adzawaipsa, ndi kuwasyasyalika; koma anthu akudziwa Mulungu wao adzalimbika mtima, nadzachita mwamphamvu.


Ndipo pakugwa iwo adzathandizidwa ndi thandizo laling'ono; koma ambiri adzaphatikizana nao ndi mau osyasyalika.


Koma apo pophukira mizu yake adzauka wina m'malo mwake, ndiye adzafika kulimbana nalo khamu la nkhondo, nadzalowa m'linga la mfumu ya kumpoto, nadzachita molimbana nao, nadzawagonjetsa;


Chitsutso ichi adachilamulira amithenga oyerawo, anachifunsa, nachinena, kuti amoyo adziwe kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna, nauutsira wolubukira anthu.


Ndinali kulingilirira za nyangazi, taonani, pakati pa izo panaphuka nyanga ina, ndiyo yaing'ono; patsogolo pake zitatu za nyanga zoyambazi zinazulidwa ndi mizu yomwe; ndipo taonani, m'nyanga m'menemo munali maso ngati maso a munthu, ndi pakamwa palikunena zazikulu.


Ndipo potsiriza pake pa ufumu wao, atakwanira olakwa, idzauka mfumu ya nkhope yaukali yakuzindikira zinsinsi.


Ndipo mwa kuchenjera kwake adzapindulitsa chinyengo m'dzanja mwake, nadzadzikuza m'mtima mwake; ndipo posatekeseka anthu, adzaononga ambiri; adzaukiranso kalonga wa akalonga, koma adzathyoledwa popanda dzanja.


Ndipo mu imodzi ya izi munaphuka nyanga yaing'ono, imene inakula kwakukulu ndithu, kuloza kumwera, ndi kum'mawa, ndi kudziko lokometsetsa.


Ndipo Yehova walamulira za iwe kuti asabzalidwenso ena a dzina lako; m'nyumba ya milungu yako ndidzachotsa fano losema ndi fano loyenga; ndidzakukonzerapo manda, pakuti iwe ndiwe wopepuka.


Popeza ndinamuuza kuti ndidzaweruza nyumba yake kosatha chifukwa cha zoipa anazidziwa, popeza ana ake anadzitengera temberero, koma iye sanawaletse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa