Masalimo 101:6 - Buku Lopatulika Maso anga ayang'ana okhulupirika m'dziko, kuti akhale ndi Ine; iye amene ayenda m'njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Maso anga ayang'ana okhulupirika m'dziko, kuti akhale ndi Ine; iye amene ayenda m'njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma anthu okhulupirika am'dziko, ndidzaŵayang'ana moŵakomera mtima, ndipo adzakhala ndi ine. Oyenda m'njira yopanda cholakwa adzanditumikira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Maso anga adzakhala pa okhulupirika mʼdziko, kuti akhale pamodzi ndi ine; iye amene mayendedwe ake ndi wosalakwa adzanditumikira. |
M'maso mwake munthu woonongeka anyozeka; koma awachitira ulemu akuopa Yehova. Atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ai.
natenge miyala ina, naikhazike m'malo mwa miyala ija; natenge dothi lina, namatenso nyumbayo.
Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang'anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthawi yake?
Ngati wina anditumikira Ine, anditsate; ndipo kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Ngati wina anditumikira Ine, Atate adzamchitira ulemu iyeyu.
Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.
Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi.
Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;