Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Marko 7:3 - Buku Lopatulika

Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse sakudya osasamba m'manja ao, kuti asungire mwambo wa akulu;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse sakudya osasamba m'manja ao, kuti asungire mwambo wa akulu;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pajatu Afarisi ndi Ayuda ena onse saadya asanasambe m'manja mwa njira yoyenera. Amatero kuti asunge mwambo wa makolo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

(Afarisi ndi Ayuda onse sadya pokhapokha atasamba mʼmanja, kusunga mwambo wa makolo awo.

Onani mutuwo



Marko 7:3
10 Mawu Ofanana  

muyesa achabe mau a Mulungu mwa mwambo wanu, umene munaupereka: ndi zinthu zotere zambiri muzichita.


Ndipo Afarisi ndi alembi anamfunsa Iye, kuti, Bwanji ophunzira anu satsata mwambo wa akulu, koma akudya mkate wao ndi m'manja mwakuda?


Ndipo anazizwa Mfarisiyo, pakuona kuti anayamba chakudya asanasambe.


Ndipo panali pamenepo mitsuko yamiyala isanu ndi umodzi yoikidwako monga mwa mayeretsedwe a Ayuda, yonse ya miyeso iwiri kapena itatu.


ndipo ndinawaposa ndi kutsogola mwa Chiyuda ambiri a msinkhu wanga mwa mtundu wanga, ndipo ndinakhala wachangu koposa pa miyambo ya makolo anga.


Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Khristu;


podziwa kuti simunaomboledwa ndi zovunda, golide ndi siliva, kusiyana nao makhalidwe anu achabe ochokera kwa makolo anu: