Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 7:13 - Buku Lopatulika

13 muyesa achabe mau a Mulungu mwa mwambo wanu, umene munaupereka: ndi zinthu zotere zambiri muzichita.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 muyesa achabe mau a Mulungu mwa mwambo wanu, umene munaupereka: ndi zinthu zotere zambiri muzichita.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Pakutero mau a Mulungu inu mumaŵasandutsa achabechabe, chifukwa cha mwambo wanu umene mumasiyirana. Ndipo mumachita zinanso zambiri zotere.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Potero mumachepetsa mawu a Mulungu kukhala wopanda mphamvu ndi miyambo yanu imene mumapatsirana. Ndipo mumachita zinthu zina zambiri monga zimenezi.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 7:13
14 Mawu Ofanana  

Kuchilamulo ndi kuumboni! Ngati iwo sanena malinga ndi mau awa, ndithu sadzaona mbandakucha.


Taona tsono, yemweyo akabala mwana uyu, naona zochimwa zonse adazichita atate wake, naopa wosachita zoterezo,


Ndinamlembera zinthu zambirimbirizo za chilamulo changa, koma zinayesedwa ngati chinthu chachilendo.


iyeyo sadzalemekeza atate wake. Ndipo inu mupeputsa mau a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu.


simulolanso kumchitira kanthu atate wake kapena amai wake;


Ndipo anadziitaniranso khamu la anthu, nanena nao, Mverani Ine nonsenu, ndipo dziwitsani:


Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse sakudya osasamba m'manja ao, kuti asungire mwambo wa akulu;


Ndipo Afarisi ndi alembi anamfunsa Iye, kuti, Bwanji ophunzira anu satsata mwambo wa akulu, koma akudya mkate wao ndi m'manja mwakuda?


Ndipo ananena nao, Bwino mukaniza lamulo la Mulungu, kuti musunge mwambo wanu.


ndipo ndinawaposa ndi kutsogola mwa Chiyuda ambiri a msinkhu wanga mwa mtundu wanga, ndipo ndinakhala wachangu koposa pa miyambo ya makolo anga.


njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.


osasamala nthano zachabe za Chiyuda, ndi malamulo a anthu opatuka kusiyana nacho choonadi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa