Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 7:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo anadziitaniranso khamu la anthu, nanena nao, Mverani Ine nonsenu, ndipo dziwitsani:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo anadziitaniranso khamu la anthu, nanena nao, Mverani Ine nonsenu, ndipo dziwitsani:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Pambuyo pake Yesu adaitananso anthu aja kuti adze pafupi, ndipo adaŵauza kuti, “Mverani nonsenu, ndipo mumvetse bwino.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Yesu anayitananso gulu la anthu ndipo anati, “Tandimverani nonsenu, ndipo zindikirani izi.

Onani mutuwo Koperani




Marko 7:14
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni Iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anamuyankha.


Ndipo Mikaya anati, Mukabwera ndithu ndi mtendere Yehova sanalankhule mwa ine. Nati, Mvetsani, anthu inu nonse.


Zindikirani, opulukira inu mwa anthu; ndipo opusa inu, mudzachita mwanzeru liti?


Achibwana inu, chenjerani, opusa inu, khalani ndi mtima wozindikira;


Ndipo Iye anati, Kauze anthu awa, Imvani inu ndithu, koma osazindikira; yang'anani inu ndithu, koma osadziwitsa.


amene mneneri Yeremiya ananena kwa anthu onse a Yuda, ndi onse okhala mu Yerusalemu, kuti,


Ndipo Iye anaitana makamuwo nati kwa iwo, Imvani, nimudziwitse;


muyesa achabe mau a Mulungu mwa mwambo wanu, umene munaupereka: ndi zinthu zotere zambiri muzichita.


kulibe kanthu kunja kwa munthu kukalowa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zakutuluka mwa munthu, ndizo zakumdetsa munthu.


Pomwepo pamene anthu a zikwizikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, Iye anayamba kunena kwa ophunzira ake poyamba, Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi, chimene chili chinyengo.


Ndipo Filipo anamthamangira, namva iye alikuwerenga Yesaya mneneri, ndipo anati, Kodi muzindikira chimene muwerenga?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa