Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 7:15 - Buku Lopatulika

15 kulibe kanthu kunja kwa munthu kukalowa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zakutuluka mwa munthu, ndizo zakumdetsa munthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 kulibe kanthu kunja kwa munthu kukalowa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zakutuluka mwa munthu, ndizo zakumdetsa munthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Palibe chinthu chochokera kunja ndi kuloŵa m'kati mwa munthu chimene chingathe kumuipitsa. Koma zimene zimatuluka mwa munthu ndizo zimamuipitsa.” [

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Palibe kanthu kunja kwa munthu kamene kakalowa mwa iye kangamusandutse wodetsedwa. Koma zimene zituluka mwa munthu ndizo zimupanga kukhala wodetsedwa.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 7:15
17 Mawu Ofanana  

Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.


Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? Pakuti m'kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.


Ndipo Iye anati, Kodi inunso mukhala chipulukirire?


Ndipo anadziitaniranso khamu la anthu, nanena nao, Mverani Ine nonsenu, ndipo dziwitsani:


ndipo anati kwa iwo, Mudziwa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu Myuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wa mtundu wina; koma Mulungu anandionetsera ine ndisanenere aliyense ali munthu wamba kapena wonyansa;


Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.


Chonse chogulitsidwa pa msika wa nyama, mudye, osafunsa kanthu chifukwa cha chikumbumtima;


Zonse ziyera kwa iwo amene ayera mtima; koma kwa iwo odetsedwa ndi osakhulupirira kulibe kanthu koyera; komatu zadetsedwa nzeru zao ndi chikumbumtima chao.


Musatengedwe ndi maphunzitso a mitundumitundu, ndi achilendo; pakuti nkokoma kuti mtima ukhazikike ndi chisomo; kosati ndi zakudya, zimene iwo adazitsata sanapindule nazo.


Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyanasiyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa