Marko 15:3 - Buku Lopatulika Ndipo ansembe aakulu anamnenera Iye zinthu zambiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ansembe aakulu anamnenera Iye zinthu zambiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Akulu a ansembe aja adayamba kumneneza zambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Akulu a ansembe anamunenera zinthu zambiri. |
Iye anatsenderezedwa koma anadzichepetsa yekha osatsegula pakamwa pake; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwanawankhosa amene ali duu pamaso pa omsenga, motero sanatsegule pakamwa pake.
Ndipo Pilato anamfunsa Iye, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo anayankha, nanena naye, Mwatero.
Ndipo Pilato anamfunsanso, nanena, Suyankha kanthu kodi? Taona, akunenera Iwe zinthu zambiri zotere.
Pa ichi Pilato anafuna kumasula Iye; koma Ayuda anafuula, ndi kunena, Ngati mumasula ameneyo, simuli bwenzi la Kaisara; yense wodziyesera yekha mfumu atsutsana naye Kaisara.