Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 15:5 - Buku Lopatulika

5 Koma Yesu sanayankhenso kanthu; kotero kuti Pilato anazizwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Koma Yesu sanayankhenso kanthu; kotero kuti Pilato anazizwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Koma Yesu sadayankhenso kanthu, kotero kuti Pilato adadabwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Koma Yesu sanayankhebe, ndipo Pilato anadabwa.

Onani mutuwo Koperani




Marko 15:5
10 Mawu Ofanana  

Ndikhala chodabwitsa kwa ambiri; koma Inu ndinu pothawira panga polimba.


Iye anatsenderezedwa koma anadzichepetsa yekha osatsegula pakamwa pake; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwanawankhosa amene ali duu pamaso pa omsenga, motero sanatsegule pakamwa pake.


Taonani, ine ndi ana amene Yehova wandipatsa ine, tili zizindikiro ndi zodabwitsa mwa Israele, kuchokera kwa Yehova wa makamu, amene akhala m'phiri la Ziyoni.


Tamvera tsono, Yoswa mkulu wa ansembe, iwe ndi anzako akukhala pansi pamaso pako; pakuti iwo ndiwo chizindikiro; pakuti taonani, ndidzafikitsa mtumiki wanga, ndiye Mphukira.


Ndipo pakumnenera Iye ansembe aakulu ndi akulu, Iye sanayankhe kanthu.


Ndipo sanayankhe Iye, ngakhale mau amodzi, kotero kuti kazembe anazizwa ndithu.


Ndipo Pilato anamfunsanso, nanena, Suyankha kanthu kodi? Taona, akunenera Iwe zinthu zambiri zotere.


Ndipo anamfunsa Iye mau ambiri; koma Iye sanamyankhe kanthu.


Ndipo analowanso ku Pretorio, nanena kwa Yesu, Muchoka kuti? Koma Yesu sanamyankhe kanthu.


Pakuti ndiyesa, kuti Mulungu anaoneketsa ife atumwi otsiriza, monga titi tife; pakuti takhala ife choonetsedwa kudziko lapansi, ndi kwa angelo, ndi kwa anthu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa