Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:
Marko 1:4 - Buku Lopatulika Yohane anadza nabatiza m'chipululu, nalalikira ubatizo wa kutembenuka mtima wakuloza ku chikhululukiro cha machimo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yohane anadza nabatiza m'chipululu, nalalikira ubatizo wa kutembenuka mtima wakuloza ku chikhululukiro cha machimo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zimenezi zidachitikadi pamene Yohane Mbatizi adaafika ku chipululu, nayamba kulalika. Ankauza anthu kuti, “Tembenukani mtima, mubatizidwe, ndipo Mulungu adzakukhululukirani machimo anu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Yohane anabwera mʼmadera a mʼchipululu nabatiza, ndi kulalikira za ubatizo wa kutembenuka mtima ndi wa chikhululukiro cha machimo. |
Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto:
Ndipo anatuluka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a ku Yerusalemu onse; nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje Yordani, powulula machimo ao.
Ndipo Yohane analinkubatiza mu Ainoni pafupi pa Salimu, chifukwa panali madzi ambiri pamenepo; ndipo analinkufikako anthu, nalinkubatizidwa.
mauwo muwadziwa inu, adadzawo ku Yudeya lonse, akuyamba ku Galileya, ndi ubatizo umene Yohane anaulalikira;
Ndipo tsopano uchedweranji? Tauka, nubatizidwe ndi kusamba kuchotsa machimo ako, nuitane pa dzina lake.