Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 3:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo Yohane analinkubatiza mu Ainoni pafupi pa Salimu, chifukwa panali madzi ambiri pamenepo; ndipo analinkufikako anthu, nalinkubatizidwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo Yohane analinkubatiza m'Ainoni pafupi pa Salimu, chifukwa panali madzi ambiri pamenepo; ndipo analinkufikako anthu, nalinkubatizidwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Yohane nayenso ankabatiza ku Ainoni pafupi ndi Salimu, chifukwa kumeneko kunali madzi ambiri. Anthu ankafikako, iye nkumaŵabatiza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Ndipo Yohane amabatizanso ku Ainoni kufupi ndi Salimu, chifukwa kumeneko kunali madzi ambiri ndipo anthu amabwererabwererabe kudzabatizidwa.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 3:23
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anafika ndi mtendere kumzinda wa Sekemu umene uli m'dziko la Kanani, pamene anachokera ku Padanaramu; namanga tsasa pandunji pa mzindapo.


Iwe wokhala pamadzi ambiri, wochuluka chuma, chimaliziro chako chafika, chilekezero cha kusirira kwako.


Mai wako ananga mpesa wookedwa kumadzi; muja anakhala mumtendere unabala zipatso, wodzala ndi nthambi, chifukwa cha madzi ambiri.


ndipo taonani, ulemerero wa Mulungu wa Israele unadzera njira ya kum'mawa, ndi mau ake ananga mkokomo wa madzi ambiri, ndi dziko linanyezimira ndi ulemerero wake.


Chifukwa chake iye ananena kwa makamuwo a anthu amene anatulukira kukabatizidwa ndi iye, Obadwa a njoka inu, anakulangizani inu ndani kuthawa mkwiyo ulinkudza?


Zitapita izi anadza Yesu ndi ophunzira ake kudziko la Yudeya; ndipo pamenepo anatsotsa nao pamodzi, nabatiza.


Pakuti Yohane sanaikidwe m'ndende.


ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira, ngati woyengeka m'ng'anjo; ndi mau ake ngati mkokomo wa madzi ambiri.


Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndi ngati mau a bingu lalikulu; ndipo mau amene ndinawamva anakhala ngati a azeze akuimba azeze ao;


Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, ndi kunena, Aleluya; pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.


Ndipo anapyola dziko lamapiri la Efuremu, napyola dziko la Salisa, koma sanawapeze; pamenepo anapyolanso dziko la Salimu, koma panalibe pamenepo, napyola dziko la Abenjamini, osawapeza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa