Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Luka 9:5 - Buku Lopatulika

Ndipo onse amene sakakulandireni inu, m'mene mutuluka m'mudzi womwewo, sansani fumbi la pa mapazi anu, likhale mboni ya paiwo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo onse amene sakakulandireni inu, m'mene mutuluka m'mudzi womwewo, sansani fumbi la pa mapazi anu, likhale mboni ya paiwo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ngati kumudzi kwina anthu sakulandirani, pochoka kumeneko musanse fumbi la kumapazi kwanu. Limeneli likhale chenjezo kwa iwowo.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ngati anthu sakulandirani, sasani fumbi la kumapazi anu pomwe mukuchoka mu mzinda wawo ngati umboni owatsutsa.”

Onani mutuwo



Luka 9:5
13 Mawu Ofanana  

Ndinakutumulanso malaya anga, ndi kuti, Mulungu akutumule momwemo munthu yense wosasunga mau awa, kunyumba yake, ndi kuntchito yake; inde amkutumule momwemo, namtayire zake zonse. Ndi msonkhano wonse unati, Amen, nalemekeza Yehova. Ndipo anthu anachita monga mwa mau awa.


ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha Ine, kukhala mboni ya kwa iwo, ndi kwa anthu akunja.


Ndipo pamalo ponse sakulandirani, kapena kumvera inu, pakuchoka kumeneko, sansani fumbi lili kumapazi anu, likhale mboni ya kwa iwo.


Munthu aliyense adzalandira kamodzi ka tiana totere chifukwa cha dzina langa, alandira Ine; ndipo yense amene akalandira Ine, salandira Ine, koma Iye amene anandituma Ine.


Iye wakumvera inu, andimvera Ine; ndipo iye wakukana inu, andikana Ine; ndipo iye wakukana Ine amkana Iye amene anandituma Ine.


Ndipo Iye anamuuzitsa, kuti asanene kwa munthu aliyense; koma uchoke, nudzionetse wekha kwa wansembe, nupereke nsembe ya pa chikonzedwe chako, monga adalamulira Mose, kukhale umboni kwa iwo.


Ndipo m'nyumba iliyonse mukalowemo, khalani komweko, ndipo muzikachokera kumeneko.


Amene aliyense akalandire kamwana aka m'dzina langa alandira Ine; ndipo amene andilandira Ine alandira Iye amene anandituma Ine; pakuti iye wakukhala wamng'onong'ono wa inu nonse, yemweyu ndiye wamkulu.


Koma iwo, m'mene adawasansira fumbi la ku mapazi ao anadza ku Ikonio.


Koma pamene iwo, anamkana, nachita mwano, anakutumula malaya ake, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndilibe kanthu; kuyambira tsopano ndinka kwa amitundu.