Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho?
Luka 3:12 - Buku Lopatulika Ndipo amisonkho omwe anadza kudzabatizidwa, nati kwa iye, Mphunzitsi, ife tizichita chiyani? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo amisonkho omwe anadza kudzabatizidwa, nati kwa iye, Mphunzitsi, ife tizichita chiyani? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kudabweranso okhometsa msonkho kuti Yohane aŵabatize. Iwo adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi ife tizichita zabwino zanji?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amisonkho nawonso anabwera kudzabatizidwa. Iwo anafunsa kuti, “Aphunzitsi, ife tichite chiyani?” |
Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho?
Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafune kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa.
Ndipo anthu onse ndi amisonkho omwe, pakumva, anavomereza kuti Mulungu ali wolungama, popeza anabatizidwa iwo ndi ubatizo wa Yohane.
Koma pamene anamva ichi, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndi atumwi enawo, Tidzachita chiyani, amuna inu, abale?